9
Yehova Aonekera Solomoni
Solomoni atatsiriza kumanga Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndi kukwaniritsa kuchita zonse zimene ankafuna, Yehova anamuonekera kachiwiri, monga momwe anamuonekera ku Gibiyoni. Yehova ananena kwa iye kuti:
“Ndamva pemphero ndi pembedzero lako pa zimene wapempha pamaso panga. Ndayipatula Nyumba iyi, imene wamanga, poyikamo Dzina langa mpaka muyaya. Maso anga ndi mtima wanga zidzakhala pamenepo nthawi zonse.
“Kunena za iwe, ukayenda pamaso panga mokhulupirika, mwangwiro ndi moona mtima monga momwe anachitira abambo ako Davide, ndi kuchita zonse zimene ndakulamula ndi kusamalitsa malangizo ndi malamulo anga, Ine ndidzakhazikitsa mpando wako waufumu pa Israeli mpaka muyaya, monga ndinalonjezera abambo ako Davide pamene ndinati, ‘Sipadzasowa munthu pa mpando waufumu wa Israeli.’
“Koma ngati iwe kapena ana ako mudzapatuka ndi kuleka kusunga malamulo ndi mawu anga amene ndakupatsani ndi kupita kukatumikira milungu ina ndi kuyipembedza, pamenepo Ine ndidzazula Aisraeli mʼdziko limene ndinawapatsa ndiponso ndidzayikana Nyumba ino imene ndayipatula chifukwa cha Dzina langa. Pamenepo Aisraeli adzasanduka mwambi ndi chinthu chonyozedwa pakati pa anthu onse. Ndipo ngakhale kuti tsopano Nyumba ya Mulunguyi ndi yokongola kwambiri, onse amene adzadutsa pano adzadabwa kwambiri ndipo adzatsonya ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere mʼdziko muno ndi pa Nyumba ya Mulunguyi?’ Anthu adzayankha kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti asiya Yehova Mulungu wawo amene anatulutsa makolo awo mʼdziko la Igupto, ndipo akangamira milungu ina ndi kumayipembedza ndi kuyitumikira. Choncho Iye wabweretsa zovuta zonsezi.’ ”
Zina zimene Solomoni Anachita
10 Patatha zaka makumi awiri, ndiye nthawi imene Solomoni anamanga nyumba ziwirizi: Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, 11 Mfumu Solomoni anapereka mizinda makumi awiri ya ku Galileya kwa Hiramu mfumu ya ku Turo chifukwa Hiramu nʼkuti atapereka mitengo yonse ya mkungudza ndi ya payini ndiponso golide yense zimene Solomoni ankazifuna. 12 Koma Hiramu atabwera kuchokera ku Turo kudzaona mizinda imene Solomoni anamupatsa, sanasangalatsidwe nayo mizindayo. 13 Iye anafunsa kuti, “Mʼbale wanga, kodi iyi nʼkukhala mizinda yondipatsa?” Ndipo iye anayitcha mizindayo Dziko la Kabuli, dzina lomwe amatchedwa mpaka lero lino. 14 Koma Hiramu anali atatumiza kwa mfumu golide oposa makilogalamu 4,000.
15 Izi ndi zimene anachita Mfumu Solomoni: Analamula anthu kuti agwire ntchito yathangata pomanga Nyumba ya Yehova, nyumba yake, malo achitetezo a Milo, mpanda wa Yerusalemu, Hazori, Megido ndi Gezeri. 16 (Farao mfumu ya ku Igupto inali itathira nkhondo ndi kulanda Gezeri. Iye anatentha mzindawo. Anapha Akanaani amene ankakhala mʼmenemo ndipo kenaka anawupereka ngati mphatso yaukwati kwa mwana wake wamkazi amene anakwatiwa ndi Solomoni. 17 Ndipo Solomoni anamanganso Gezeri.) Iye anamanga Beti-Horoni Wakumunsi, 18 Baalati ndi Tadimori ku chipululu, mʼdziko lake lomwelo, 19 pamodzinso ndi mizinda yake yosungira chuma ndiponso mizinda yosungiramo magaleta ndi akavalo ake. Anamanganso chilichonse chimene anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene iye ankalamulira.
20 Panali anthu amene anatsala pakati pa mitundu ya Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi (anthu awa sanali Aisraeli). 21 Zimenezi ndiye zinali zidzukulu zawo zotsalira mʼdzikoli, anthu amene Aisraeli sanathe kuwawononga kotheratu. Solomoni anawatenga ndi kukhala akapolo ake ogwira ntchito yathangata, monga zilili mpaka lero lino. 22 Koma Solomoni sanagwiritse ntchito ya ukapolo Mwisraeli aliyense; iwo anali anthu ake ankhondo, nduna zake, atsogoleri a ankhondo, akapitawo ake, olamulira magaleta ndi oyendetsa magaleta ake. 23 Amenewa ndiwo anali akuluakulu oyangʼanira ntchito za Solomoni. Anthu okwana 550 ndiwo ankayangʼanira anthu amene ankagwira ntchitowo.
24 Mwana wamkazi wa Farao atachoka mu Mzinda wa Davide, kupita ku nyumba ya mfumu imene Solomoni anamumangira, Solomoni anamanga malo achitetezo a Milo.
25 Katatu pa chaka Solomoni ankapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pa guwa lansembe limene anamangira Yehova ndiponso ankafukiza lubani pamaso pa Yehova. Potero ankakwaniritsa zoyenera kuchitika mu Nyumba ya Yehova.
26 Mfumu Solomoni anapanganso sitima zapamadzi ku Ezioni Geberi, malo amene ali pafupi ndi Eloti ku Edomu, mʼmbali mwa Nyanja Yofiira. 27 Ndipo Hiramu anatumiza anthu ake oyendetsa sitima zapamadzi amene ankadziwa za pa nyanja kuti aziyendetsa pamodzi ndi anthu a Solomoni. 28 Iwo anapita ku Ofiri ndipo anakatenga golide okwana makilogalamu 14,000, amene anamupereka kwa Mfumu Solomoni.