2
Malangizo Achipembedzo
1 Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika. 2 Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima. 3 Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu, 4 amene amafuna kuti anthu onse apulumutsidwe ndipo kuti adziwe choonadi. 5 Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu. 6 Iyeyu anadzipereka kukhala dipo lowombolera anthu onse. Umenewu ndi umboni umene waperekedwa mu nthawi yake yoyenera. 7 Nʼchifukwa chake anandisankha kukhala mlaliki ndiponso mtumwi wophunzitsa anthu a mitundu ina mawu achikhulupiriro choona. Sindikunama ayi, ndikunena zoona.
8 Choncho ndikufuna kuti paliponse popemphera, amuna azikweza manja awo kwa Mulungu mopanda mkwiyo kapena kukangana.
9 Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali. 10 Koma adzikongoletse ndi ntchito zabwino zoyenera mayi wopembedza Mulungu.
11 Amayi azikhala chete pophunzitsidwa ndi mtima ogonjera kwathunthu. 12 Ine sindikulola kuti amayi aziphunzitsa kapena kulamulira amuna; koma akhale chete. 13 Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa kenaka Hava. 14 Ndipo Adamu si amene ananyengedwa koma mkazi ndiye amene ananyengedwa nachimwa. 15 Ndipo mkazi adzapulumutsidwa pobereka mwana ngati apitiriza kukhala mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkuyera mtima pamodzi ndi kudzichepetsa konse.