KALATA YACHIWIRI YA
PETRO
1
1 Ndine Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu.
Kwa anthu amene analandira chikhulupiriro cha mtengowapatali chomwe ifenso tinalandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.
2 Chisomo ndi mtendere zochuluka zikhale nanu pomudziwa Mulungu ndi Yesu Ambuye athu.
Kudziwa za Mayitanidwe ndi za Kusankhidwa Kwathu
3 Mulungu mwa mphamvu zake anatipatsa zonse zofunika kukhala moyo opembedza, potidziwitsa za Iyeyo amene anatiyitana ku ulemerero wake ndi ubwino wake. 4 Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili mʼdziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa.
5 Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa chikhulupiriro chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru. 6 Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu. 7 Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi. 8 Ngati zonsezi zikhala mwa inu nʼkumachuluka, zidzakuthandizani kuti musakhale aulesi ndi osapindula ndi chidziwitso chanu cha Ambuye athu Yesu Khristu. 9 Koma ngati wina alibe zimenezi, ndi wakhungu sangathe kuona patali, ndipo wayiwala kuti anayeretsedwa machimo ake akale.
10 Nʼchifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi, simudzagwa konse. 11 Mudzalandiridwa bwino kwambiri mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.
Kukhala Oyera Mtima
12 Tsono ine ndidzakukumbutsani nthawi zonse za zinthu zimenezi, ngakhale kuti mumazidziwa ndipo kuti munakhazikika mʼchoonadi chimene muli nacho tsopano. 13 Ndikuganiza kuti nʼkoyenera ndikanali mu msasa uno, kuti ndikutsitsimutseni ndi kukukumbutsani, 14 chifukwa ndikudziwa kuti posachedwapa ndikuchoka mu msasa uno, monga Ambuye athu Yesu Khristu anandidziwitsiratu. 15 Ndipo ndidzayesetsa kuti nditachoka, mudzakumbukire nthawi zonse.
16 Ife sitinatsate nkhani zongopeka titakuwuzani za mphamvu zake ndi zakubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu, koma tinaona ndi maso athu za ukulu wake. 17 Pakuti Iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate atamufikira mawu ochokera ku ulemerero wa ukulu akuti, “Uyu ndi mwana wanga amene Ine ndimukonda, amene ndimakondwera naye kwambiri.” 18 Ifeyo tinamva mawuwa akuchokera kumwamba pamene tinali naye pamodzi pa phiri lopatulika lija.
19 Tsono ifenso tili ndi mawu a uneneri amene ndi odalirika kwambiri ndipo inu mudzachita bwino mukawasamalira mawuwa, monga kuwunika kumene kukuwala mu mdima, mpaka tsiku lidzayambe kucha, pamene nthanda idzayambe kuwala mʼmitima mwanu. 20 Kuposa zonse, inu muyenera kuzindikira kuti palibe mawu a uneneri amene amatanthauzidwa pa okha. 21 Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.