Mlaliki
1
Zapansipano Nʼzopandapake
1 Mawu a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu:
2 “Zopandapake! Zopandapake!”
atero Mlaliki.
“Zopandapake kotheratu!
Zopandapake.”
3 Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zake zonse
zimene amasautsidwa nazo pansi pano?
4 Mibado imabwera ndipo mibado imapita,
koma dziko lapansi limakhalapobe nthawi zonse.
5 Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa
ndipo limapita mwamsanga kumene limatulukira.
6 Mphepo imawombera cha kummwera
ndi kukhotera cha kumpoto;
imawomba mozungulirazungulira,
kumangobwererabwerera komwe yachokera.
7 Mitsinje yonse imakathira ku nyanja,
koma nyanjayo sidzaza;
kumene madziwo amachokera,
amabwereranso komweko.
8 Zinthu zonse ndi zotopetsa,
kutopetsa kwake ndi kosaneneka.
Maso satopa ndi kuona
kapena khutu kukwaniritsidwa ndi kumva.
9 Zomwe zinalipo kale zidzakhalaponso,
zomwe zinachitika kale zidzachitikanso.
Ndiye kuti chatsopano palibiretu pansi pano.
10 Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti,
“Taona! Ichi ndiye chatsopano?”
Chinalipo kale, kalekale;
chinalipo ife kulibe.
11 Anthu akale sakumbukiridwa,
ngakhale amene adzabwera mʼtsogolomu
sadzakumbukiridwa ndi iwo
amene adzabwere pambuyo pawo.
Nzeru Nʼzopandapake
12 Ine, Mlalikine, ndinali mfumu ya Israeli mu Yerusalemu. 13 Ndinayika mtima wanga pophunzira ndi kufunafuna mwa nzeru zinthu zonse zimene zimachitika pansi pa thambo. Ndi ntchito yolemetsa ndithu imene Mulungu anayipereka kwa anthu! 14 Ine ndaona zinthu zonse zochitika pansi pano; zinthu zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
15 Chinthu chokhota sichingathe kuwongoledwa;
chimene palibe sichingathe kuwerengedwa.
16 Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Taona, ine ndakula ndi kukhala wa nzeru zochuluka kupambana aliyense amene analamulirapo Yerusalemu ndisanabadwe; ndaphunzira nzeru zochuluka ndi luntha.” 17 Ndipo ndinadzipereka kuti ndithe kumvetsa kuti nzeru nʼchiyani, misala nʼchiyani, uchitsiru nʼchiyani, koma ndinazindikira ichi, kuti kuteronso nʼkungodzivuta chabe.
18 Pakuti nzeru zochuluka zimabweretsa chisoni chochulukanso:
chidziwitso chochuluka, zowawa zochulukanso.