49
Uthenga Wonena za Aamoni
1 Yehova ananena izi:
Amoni,
“Kodi Israeli alibe ana aamuna?
Kapena alibe mlowamʼmalo?
Tsono nʼchifukwa chiyani anthu opembedza Moleki alanda dziko la Gadi?
Nʼchifukwa chiyani anthu ake akukhala mʼmizinda ya Gadi?
2 Koma nthawi ikubwera,”
akutero Yehova,
“pamene ndidzamveketse mfuwu wankhondo
ku Raba, likulu la Amoni;
ndipo malo awo opembedzera milungu yawo
adzatenthedwa ndi moto.
Choncho Aisraeli adzalandanso dziko lawo
kuchokera kwa amene anawalanda poyamba dzikolo,”
akutero Yehova.
3 “Lirani, inu anthu a ku Hesiboni chifukwa wowononga uja wafika!
Fuwulani, inu anthu okhala ku Raba!
Valani ziguduli ndi kulira mwamphamvu;
thamangani uku ndi uku mʼkati mwa malinga,
chifukwa mulungu wanu Moleki adzapita ku ukapolo,
pamodzi ndi ansembe ake ndiponso akuluakulu ake.
4 Chifukwa chiyani mukunyadira
chigwa chanu,
inu anthu osakhulupirika
amene munadalira chuma chanu nʼkumati:
‘Ndani angandithire nkhondo?’
5 Ndidzabweretsa zoopsa pa iwe
zochokera kwa onse amene akuzungulira,”
akutero Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse.
“Mudzathawa, ndipo aliyense adzathawitsa moyo wake.
Sipadzapezeka munthu wosonkhanitsanso othawawo.
6 “Komabe pambuyo pake, ndidzabwezera kwawo Aamoni,”
akutero Yehova.
Uthenga Wonena za Edomu
7 Yehova Wamphamvuzonse ananena izi za Edomu:
“Kodi nzeru sizikupezekanso ku Temani?
Kodi anzeru analeka kupereka uphungu?
Kodi nzeru zawo zinatheratu?
8 Inu anthu a ku Dedani, thawani,
bwererani ndi kukabisala ku makwalala
chifukwa ndidzagwetsa mavuto pa zidzukulu za Esau
popeza nthawi yawo ya chiweruzo yafika.
9 Kodi anthu othyola mphesa akanafika kwa inu
akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha?
Anthu akuba akanafika usiku
akanangotengako zimene akuzifuna zokha?
10 Koma ine ndazivula zidzukulu za Esau.
Ndaonetsa poyera malo awo obisalamo,
kotero kuti sadzathanso kubisala.
Ana ake, abale ake pamodzi ndi anansi ake awonongeka.
Palibe wonena kuti,
11 ‘Siyani ana anu amasiye; Ine ndidzawateteza.
Amayi anu amasiye akhoza kudalira Ine.’ ”
12 Yehova akuti, “Ngati iwo amene sanali oyenera kulangidwa adzamwa chikho cha chiweruzo, ndiye muyesa kuti inuyo simudzalangidwa? Ayi ndithu simudzakhala osalangidwa. Mudzamwa ndithu chikhocho. 13 Ine ndikulumbira, akutero Yehova, kuti mzinda wa Bozira udzasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha, chomachiseka ndiponso chotembereredwa. Mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka muyaya.”
14 Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova:
Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti,
“Sonkhanani pamodzi kuti muthire nkhondo Edomu!
Konzekerani nkhondo!”
15 “Ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina.
Mudzakhala anthu onyozeka pakati pa anthu.
16 Kuopseza kwako kwakunyenga;
kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa,
iwe amene umakhala mʼmapanga
a mʼmatanthwe ndi mʼmapiri.
Ngakhale utamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga,
ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,”
akutero Yehova.
17 “Dziko la Edomu lidzasanduka chinthu chochititsa mantha.
Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawo
chifukwa cha kuwonongeka kwake.
18 Monga momwe anawonongekera Sodomu ndi Gomora,
pamodzi ndi mizinda yake yozungulira,”
akutero Yehova,
“motero palibe munthu
amene adzakhala mu Edomu.
19 “Monga mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yorodani
kupita ku malo a msipu wobiriwira,
Ine ndidzapirikitsa anthu a ku Edomu mwadzidzidzi kuchoka mʼdziko lawo.
Pambuyo pake ndidzawayikira owalamulira amene ndamufuna Ine.
Kodi ndani wofanana nane, ndipo angatsutsane nane ndani?
Ndipo ndi mʼbusa uti amene angalimbane nane?”
20 Nʼchifukwa chake imvani. Izi ndi zimene Ine Yehova
ndakonza zolangira anthu a ku Edomu ndi a ku Temani.
Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo
ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.
21 Akadzagwa Edomu padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera;
kulira kwawo kudzamveka mpaka ku Nyanja Yofiira.
22 Taonani, mtundu wina udzachita kuwuluka
nʼkudzatera pa Bozira ngati chiwombankhanga chimene chatambalitsa mapiko ake.
Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Edomu
idzagunda ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
Uthenga Wonena za Damasiko
23 Mawu a Yehova onena za Damasiko ndi awa:
“Anthu a ku Hamati ndi a ku Aripadi akuchita mantha
chifukwa amva nkhani yoyipa.
Mitima yawo yagwidwa ndi mantha
ndipo ali ngati muja ichitira nyanja yosakhazikika.
24 Anthu a ku Damasiko alefuka.
Abwerera mʼmbuyo kufuna kuthawa
chifukwa agwidwa ndi mantha aakulu.
Ali ndi nkhawa komanso mantha
ngati za mayi pa nthawi yake yochira.
25 Mzinda wotchuka
ndi wachikondwerero uja wasiyidwa!
26 Nʼchifukwa chake anyamata ake adzagwa mʼmisewu ndi kufa;
ankhondo ake onse adzawonongedwa tsiku limenelo,”
akutero Yehova Wamphamvuzonse.
27 “Ndidzatentha malinga a Damasiko;
moto udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.”
Uthenga Wonena za Kedara ndi Hazori
28 Mawu a Yehova onena za Kedara ndi maufumu a ku Hazori, amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawagonjetsa ndi awa:
“Nyamukani mukathire nkhondo ku Kedara.
Kawonongeni anthu a kummawako.
29 Landani matenti awo ndi nkhosa zawo,
ndiye kuti, mutenge nsalu zawo ndi katundu wawo.
Mutengenso ngamira zawo.
Anthu adzafuwula kwa iwo kuti,
‘Kuli zoopsa mbali zonse!’
30 “Thawani mofulumira!
Kabisaleni mʼmakhwawa, inu anthu ku Hazori,”
akutero Yehova.
“Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni wakukonzerani chiwembu;
wakonzekera zoti alimbane nanu.
31 “Nyamukani kathireni nkhondo mtundu wa anthu umene uli pamtendere,
umene ukukhala mosatekeseka,”
akutero Yehova,
“mzindawo ulibe zipata ngakhalenso mipiringidzo;
anthu ake amakhala pa okha.
32 Ngamira zawo zidzafunkhidwa,
ndipo makola a ngʼombe zawo adzalandidwa.
Ndidzabalalitsira ku mphepo zinayi onse amene amameta tsitsi lawo chamʼmbali.
Ndidzawagwetsera mavuto kuchokera ku mbali zonse,”
akutero Yehova.
33 “Hazori adzasanduka bwinja,
malo okhalamo nkhandwe
mpaka muyaya.
Palibe munthu amene adzayendemo.”
Uthenga Wonena za Elamu
34 Uthenga umene Yehova anapatsa mneneri Yeremiya wonena za Elamu, Zedekiya mfumu ya Yuda atangoyamba kulamulira ndi uwu:
35 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu,
umene uli chida chawo champhamvu.
36 Ndidzabweretsa mphepo zinayi pa Elamu
kuchokera ku zigawo zinayi zamlengalenga;
ndidzawabalalitsira ku mphepo zinayi,
ndipo sipadzakhala dziko
limene anthu a ku Elamu sadzafikako.
37 A ku Elamuwo ndidzachititsa mantha pamaso pa adani awo
komanso pamaso pa iwo amene akufuna kuwononga moyo wawo.
Ndidzawagwetsera mkwiyo wanga
ndipo adzakhala pa mavuto,”
akutero Yehova.
“Ndidzawapirikitsa ndi lupanga
mpaka nditawatheratu.
38 Ndidzakhazika mpando wanga waufumu ku Elamu
ndipo ndidzawononga mfumu yake pamodzi ndi akuluakulu ake,”
akutero Yehova.
39 “Komabe mʼtsogolomo ndidzabwezera
anthu a ku Elamu dziko lawo,”
akutero Yehova.