13
Yesu Asambitsa Mapazi a Ophunzira Ake
Inali pafupifupi nthawi ya phwando la Paska. Yesu anadziwa kuti nthawi yafika yoti achoke mʼdziko lapansi ndi kupita kwa Atate. Atawakonda ake amene anali mʼdziko lapansi, Iye anawaonetsa chikondi chake chonse.
Atayamba kudya mgonero, mdierekezi anali atalowa kale mu mtima wa Yudasi Isikarioti mwana wa Simoni, kuti amupereke Yesu. Yesu podziwa kuti Atate anamupatsa Iye zonse mʼmanja mwake, ndi kuti Iye anachokera kwa Mulungu ndipo amabwerera kwa Mulunguyo; anayimirira kuchoka pa chakudya navula zovala zake natenga nsalu yopukutira nadzimanga mʼchiwuno mwake. Atachita izi, anathira madzi mʼbeseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira chimene anachimanga mʼchiwuno mwake.
Atafika pa Petro, Petroyo anati kwa Iye, “Ambuye, kodi mudzandisambitsa mapazi anga?”
Yesu anayankha kuti, “Iwe sukuzindikira tsopano chimene ndikuchita, koma udzazindikira mʼtsogolo.”
Petro anati, “Ayi, Inu simudzandisambitsa konse mapazi anga.”
Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine sindisambitsa mapazi ako, ulibe gawo mwa Ine.”
Simoni Petro anayankha kuti, “Ambuye, osati mapazi okha komanso manja anga ndi mutu wanga womwe!”
10 Yesu anayankha kuti, “Munthu amene wasamba amangofunika kusamba mapazi ake okha chifukwa thupi lake lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, ngakhale kuti si aliyense mwa inu.” 11 Pakuti Iye anadziwa amene adzamupereka, ndipo nʼchifukwa chake anati saliyense wa inu ali woyera.
12 Iye atamaliza kusambitsa mapazi awo anavala zovala zake ndi kubwerera pamalo pake. Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukuzindikira zimene ndakuchitirani inu? 13  Inu mumanditcha Ine, ‘Mphunzitsi’ ndi ‘Mbuye,’ ndipo mumakhoza mukamatero, pakuti ichi ndi chimene Ine ndili. 14  Tsono ngati Ine, Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi anu. 15  Ine ndakupatsani chitsanzo kuti muzichita monga Ine ndachitira. 16  Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti wantchito saposa mbuye wake, kapena wotumidwa kuposa amene wamutuma. 17  Ngati inu mudziwa zinthu zimenezi, mudzakhala odala mukamazichita.
Yesu Aneneratu za Kuperekedwa Kwake
18  “Ine sindikunena za inu nonse. Ine ndikudziwa amene ndinawasankha. Koma izi zikukwaniritsa malemba: ‘Iye amene akudya nawo chakudya changa, ndiye amene anandiwukira.’
19  “Ine ndikukuwuzani tsopano zisanachitike zimenezi, kuti pamene zachitika, mudzakhulupirire kuti Ine Ndine. 20  Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene alandira amene Ine ndamutuma, alandiranso Ine. Aliyense amene alandira Ine, alandiranso amene anandituma.”
Yesu Aneneratu za Kuperekedwa Kwake
21 Yesu atanena izi, anavutika kwambiri mu mzimu ndipo anachitira umboni kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mmodzi mwa inu adzandipereka.”
22 Ophunzira ake anapenyetsetsana wina ndi mnzake, posadziwa kuti amanena za yani. 23 Mmodzi wa ophunzira ake amene Yesu anamukonda, anali atatsamira pachifuwa chake. 24 Simoni Petro anamukodola wophunzirayo ndi kuti, “Mufunseni akunena za yani.”
25 Atamutsamiranso Yesuyo, anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndani?”
26 Yesu anayankha kuti, “Iye amene ndidzamupatsa buledi amene ndanyema ndikususa ndi ameneyo.” Kenaka, atasunsa gawo la buledi, Iye anapereka kwa Yudasi Isikarioti, mwana wa Simoni. 27 Nthawi yomweyo Yudasi atangodya bulediyo, Satana analowa mwa Iye.
Yesu anamuwuza Iye kuti, “Chomwe ukufuna kuchita, chita msanga.” 28 Koma panalibe ndi mmodzi yemwe pa chakudyapo amene anamvetsa chifukwa chimene Yesu ananenera izi kwa iye. 29 Popeza Yudasi amasunga ndalama, ena amaganiza kuti Yesu amamuwuza iye kuti akagule zomwe zimafunika pa phwando, kapena kukapereka kanthu kena kake kwa osauka. 30 Nthawi yomweyo Yudasi atangodya buledi, anatuluka, ndipo unali usiku.
Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana
31 Yudasi atatuluka, Yesu anati, “Tsopano Mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa Iyeyu Mulungu walemekezedwanso. 32  Ngati Mulungu walemekezedwa mwa Iye, Mulungu mwini adzalemekezanso Mwana, ndipo amulemekeza nthawi yomweyo.
33  “Ana anga, Ine ndikhala nanu kwa nthawi yochepa chabe. Inu mudzandifunafuna Ine, ndipo monga momwe ndinawawuzira Ayuda, choncho Ine ndikukuwuzani tsopano kuti, kumene Ine ndikupita, inu simungabwereko.
34  “Lamulo latsopano limene ndikukupatsani ndi lakuti: Kondanani wina ndi mnzake, monga momwe Ine ndinakonda inu. Nanunso mukondane wina ndi mnzake. 35  Mukamakondana aliyense adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga.”
36 Simoni Petro anafunsa kuti, “Ambuye, kodi mukupita kuti?”
Yesu anayankha kuti, “Kumene Ine ndikupita iwe sunganditsatire tsopano, koma udzanditsatira mʼtsogolo.”
37 Petro anafunsa kuti, “Ambuye, nʼchifukwa chiyani ine sindingakutsatireni tsopano? Ine ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha Inu.”
38 Kenaka Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe udzalolera kutaya moyo chifukwa cha Ine? Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti tambala asanalire, iwe udzandikana katatu!”