15
Mpesa ndi Nthambi
1 “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndiye mwini munda. 2 Iye amadula nthambi iliyonse ya mwa Ine imene sibala chipatso, koma nthambi iliyonse imene imabala chipatso amayisadzira bwino kuti ibale zipatso zambiri. 3 Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ndayankhula inu. 4 Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku mpesa. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine.
5 “Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu. 6 Ngati wina aliyense sakhala mwa Ine, iyeyo ali ngati nthambi imene yatayidwa ndi kufota. Nthambi zotero zimatoledwa, kuponyedwa pa moto ndi kupsa. 7 Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa. 8 Atate anga amalemekezedwa mukamabereka zipatso zochuluka, ndipo potero mudzionetsa kuti ndinu ophunzira anga.
9 “Monga momwe Atate amandikondera Ine, Inenso ndakukondani. Tsopano khalani mʼchikondi changa. 10 Ngati mumvera malamulo anga, mudzakhala mʼchikondi changa, monga Ine ndimamvera malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala mʼchikondi chawo. 11 Ine ndakuwuzani izi kuti chimwemwe changa chikhale mwa Inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chokwanira. 12 Lamulo langa ndi ili: ‘Kondanani wina ndi mnzake monga Ine ndakonda inu.’ 13 Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14 Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani. 15 Ine sindikutchulaninso antchito, chifukwa wantchito sadziwa zimene bwana wake akuchita. Mʼmalo mwake Ine ndakutchani abwenzi pakuti zilizonse zimene ndinaphunzira kwa Atate, Ine ndakudziwitsani. 16 Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 17 Lamulo langa ndi ili: ‘Muzikondana.’
Dziko Lapansi Limada Ophunzira a Yesu
18 “Ngati dziko lapansi lidana nanu, dziwani kuti linayamba kudana ndi Ine. 19 Inu mukanakhala anthu a dziko lapansi, dziko lapansi likanakukondani ngati anthu ake omwe. Koma mmene zilili, inu si anthu a dziko lapansi. Ine ndakusankhani kuchokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake dziko lapansi limakudani. 20 Kumbukirani mawu amene ndinayankhula nanu akuti, ‘Palibe wantchito amene amaposa bwana wake.’ Ngati anandizunza Ine, iwo adzakuzunzaninso inu. Ngati anamvera chiphunzitso changa, iwo adzamvera chanunso. 21 Iwo adzakuchitani zimenezi chifukwa cha dzina langa, popeza sakudziwa amene anandituma Ine. 22 Ine ndikanapanda kubwera ndi kuyankhula nawo, sakanakhala ndi mlandu. Koma tsopano alibe choti nʼkukanira mlandu wawo. 23 Iye amene amadana ndi Ine amadananso Atate anga. 24 Ine ndikanapanda kuchita pakati pawo zinthu zimene wina aliyense sanachitepo, iwo sakanakhala ochimwa. Koma tsopano aona zodabwitsa izi, komabe akundida Ine pamodzi ndi Atate anga. 25 Koma zatere kuti zikwaniritse zimene zinalembedwa mʼmalamulo awo: ‘Iwo anandida Ine popanda chifukwa.’
Ntchito ya Mzimu Woyera
26 “Nkhoswe ikadzabwera imene Ine ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu Woyera wachoonadi amene achokera kwa Atate, Iyeyo adzandichitira umboni Ine. 27 Inunso mudzandichitira umboni Ine, popeza mwakhala nane kuchokera pachiyambi.”