3
Yohane Mʼbatizi
1 Mʼmasiku amenewo, Yohane Mʼbatizi anadza nalalikira mʼchipululu cha Yudeya 2 kuti, “Tembenukani mtima chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.” 3 Uyu ndi amene mneneri Yesaya ananena za iye kuti,
“Mawu a wofuwula mʼchipululu,
‘Konzani njira ya Ambuye,
wongolani njira zake.’ ”
4 Zovala za Yohane zinali zopangidwa ndi ubweya wa ngamira, ndipo amamangira lamba wachikopa mʼchiwuno mwake. Chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wa kuthengo. 5 Anthu ankapita kwa iye kuchokera ku Yerusalemu ndi ku Yudeya konse ndi ku madera onse a Yorodani. 6 Ndipo akavomereza machimo awo ankabatizidwa mu mtsinje wa Yorodani.
7 Koma iye ataona Afarisi ndi Asaduki ambiri akubwera kumene ankabatiza, anawawuza kuti, “Ana a njoka inu! Ndani anakuchenjezani kuthawa mkwiyo umene ukubwera? 8 Onetsani chipatso cha kutembenuka mtima. 9 Ndipo musaganize ndi kunena mwa inu nokha kuti, ‘Tili nawo abambo athu Abrahamu.’ Ndinena kwa inu kuti Mulungu akhoza kusandutsa miyala iyi kukhala ana a Abrahamu. 10 Tikukamba pano nkhwangwa yayikidwa kale pa mizu ya mitengo, ndipo mtengo umene subala chipatso chabwino udulidwa ndi kuponyedwa pa moto.
11 “Ine ndikubatizani ndi madzi kusonyeza kutembenuka mtima. Koma pambuyo panga akubwera wina amene ali ndi mphamvu kuposa ine, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani ndi Mzimu Woyera ndi moto. 12 Mʼdzanja lake muli chopetera ndipo adzayeretsa popunthirapo pake nadzathira tirigu wake mʼnkhokwe ndi kutentha zotsalira zonse ndi moto wosazima.”
Kubatizidwa kwa Yesu
13 Pamenepo Yesu anabwera kuchokera ku Galileya kudzabatizidwa ndi Yohane mu mtsinje wa Yorodani. 14 Koma Yohane anayesetsa kumukanira nati, “Ndiyenera kubatizidwa ndi Inu, bwanji Inu mubwera kwa ine?”
15 Yesu anayankha kuti, “Zibatero tsopano, ndi koyenera kwa ife kuchita zimenezi kukwaniritsa chilungamo chonse.” Ndipo Yohane anavomera.
16 Yesu atangobatizidwa, nthawi yomweyo potuluka mʼmadzi, kumwamba kunatsekuka ndipo taonani, Mzimu wa Mulungu anatsika ngati nkhunda natera pa Iye. 17 Ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba kuti, “Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa amene ndikondwera naye.”