CHIVUMBULUTSO
CHA YESU KHRISTU KWA YOHANE
1
Mawu Oyamba
Vumbulutso lochokera kwa Yesu Khristu, limene Mulungu anamupatsa kuti aonetse atumiki ake zimene zinayenera kuchitika posachedwa. Iye anatuma mngelo wake kuti adziwitse mtumiki wake Yohane, amene akuchitira umboni chilichonse chimene anachiona. Awa ndi Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu Khristu. Ngodala munthu amene awerenga mawu oneneratu zamʼtsogolo ndi iwo amene amamva ndi kusunga zolembedwa mʼbukuli pakuti nthawi yayandikira.
Malonje kwa Mipingo Isanu ndi Iwiri
Ndine Yohane,
Kupita ku mipingo isanu ndi iwiri ya mʼchigawo cha Asiya.
Chisomo ndi mtendere kwa inu, kuchokera kwa Iye amene ali, amene analipo ndi amene akubwera ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala patsogolo pa mpando wake waufumu, ndiponso kuchokera kwa Yesu Khristu mboni yokhulupirika, woyamba kuukitsidwa, ndi wolamulira mafumu a dziko lapansi.
 
Kwa Iye amene amatikonda ndipo watimasula ku machimo athu ndi magazi ake, ndipo watisandutsa mafumu ndi ansembe kuti tizitumikira Mulungu ndi Atate ake. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu ku nthawi zosatha, Ameni.
“Onani akubwera ndi mitambo,”
ndipo “Aliyense adzamuona,
ndi amene anamubaya omwe.”
Ndipo anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi “adzalira chingʼangʼadza chifukwa cha Iye.”
Zidzakhaladi momwemo, Ameni.
“Ine ndine Alefa ndi Omega,” akutero Ambuye Mulungu Wamphamvuzonseyo “amene muli, amene munalipo, ndi amene mudzakhalapo.”
Wina Wokhala ngati Mwana wa Munthu
Ine Yohane mʼbale wanu ndi mnzanu mʼmasautso ndi mu ufumu ndi mukupirira kwambiri, zomwe ndi zathu mwa Yesu, ndinali pa chilumba cha Patimo chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu. 10 Pa tsiku la Ambuye ndinanyamulidwa ndi Mzimu ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mawu ofuwula ngati lipenga, 11 amene anati, “Lemba mʼbuku zimene ukuziona ndipo uzitumize ku mipingo isanu ndi iwiri ya ku Efeso, Simurna, Pergamo, Tiyatira, Sarde, Filadefiya ndi ku Laodikaya.”
12 Nditatembenuka kuti ndione amene amandiyankhulayo, ndinaona zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide. 13 Pakati pa zoyikapo nyalezo ndinaona wina wooneka ngati Mwana wa Munthu atavala mkanjo wofika kumapazi ake ndipo anamangirira lamba wagolide pa chifuwa pake. 14 Tsitsi lake linali loyera ngati thonje, kuyera ngati matalala, ndipo maso ake amawala ngati malawi amoto. 15 Mapazi ake anali ngati chitsulo choti chili mʼngʼanjo yamoto, ndipo mawu ake anali ngati mkokomo wamadzi othamanga. 16 Mʼdzanja lake lamanja ananyamula nyenyezi zisanu ndi ziwiri, ndipo mʼkamwa mwake munali lupanga lakuthwa konsekonse. Nkhope yake imawala ngati dzuwa lowala kwambiri.
17 Nditamuona ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa. Kenaka Iye anasanjika dzanja lake lamanja pa ine nati, “Usachite mantha. Ndine Woyamba ndi Wotsiriza. 18  Ine ndine Wamoyo; ndinali wakufa ndipo taona ndine wamoyo mpaka muyaya! Ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi Hade.
19  “Chomwecho, lemba zimene waona, zimene zilipo panopa ndi zimene zidzachitike mʼtsogolo. 20  Tanthauzo la nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene waziona mʼdzanja langa lamanja ndi la zoyikapo nyale zagolide zisanu ndi ziwiri ndi ili: Nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndi angelo a mipingo isanu ndi iwiri ija, ndipo zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zija ndi mipingo isanu ndi iwiri ija.”