6
Kufa ku Tchimo, Kukhala ndi Moyo mwa Khristu
1 Nanga tinene chiyani? Kodi tipitirire kuchimwa kuti chisomo chichulukebe? 2 Ayi. Mʼnjira iliyonse! Popeza tinafa ku tchimo, nanga tidzapitirira bwanji kukhalabe mʼmenemo? 3 Kodi simukudziwa kuti tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu tinabatizidwa mu imfa yake? 4 Chifukwa chake ife tinayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo. Tinalowa mu imfa ndi cholinga choti monga momwe Khristu anaukitsidwa kwa akufa ndi ulemerero wa Atate, ifenso tikakhale mʼmoyo watsopano.
5 Pakuti ngati ife tinakhala amodzi ndi Iye mu imfa yake, tidzakhalanso ndithu amodzi ndi Iye mu kuuka kwake. 6 Ife tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye kuti thupi la uchimo likhale lopanda mphamvu ndi kuti tisakakhalenso akapolo a tchimo 7 chifukwa aliyense amene anafa anamasuka ku tchimo.
8 Koma ngati tinafa pamodzi ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo pamodzi ndi Iye. 9 Pakuti tikudziwa kuti popeza Khristu anaukitsidwa kwa akufa, Iye sangafenso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye. 10 Imfa imene Iye anafa, anafa ku tchimo kamodzi kokha, koma moyo umene akhala ndi wa kwa Mulungu.
11 Kotero inunso, mudzione nokha ngati akufa ku tchimo koma a moyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu. 12 Nʼchifukwa chake, musalole tchimo lilamulire matupi anu amene anafa kuti mumvere zilakolako zonyansa. 13 Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo. 14 Tchimo silidzakhalanso ndi mphamvu pa inu, chifukwa Malamulo sakulamulira moyo wanu koma chisomo.
Ife Ndife Akapolo a Mulungu
15 Nʼchiyani tsono? Kodi tidzichimwa chifukwa sitikulamulidwa ndi Malamulo koma chisomo? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! 16 Kodi inu simudziwa kuti pamene mudzipereka kwa wina wake, kumumvera ngati akapolo, ndinu akapolo a amene mumumvera? Ngati ndinu akapolo a tchimo mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo akumvera, mudzakhala olungama pamaso pake. 17 Koma ayamikidwe Mulungu pakuti ngakhale munali akapolo a tchimo, munamvera ndi mtima wonse chiphunzitso chimene munalandira. 18 Inu munamasulidwa ku tchimo ndipo tsopano mwasanduka akapolo achilungamo.
19 Ine ndikufanizira zinthu za tsiku ndi tsiku chifukwa chikhalidwe chanu nʼchofowoka. Monga momwe munkapereka ziwalo za matupi kukhala akapolo a zonyansa ndi makhalidwe oyipa, zimene zimanka zichulukirabe, choncho tsopano dziperekeni ziwalozo kuti zikhale akapolo achilungamo ndi a kuyera mtima. 20 Pomwe munali akapolo atchimo, simunkalabadira za chilungamo. 21 Kodi munapeza phindu lanji pochita zinthu zimenezi, zomwe tsopano mukuchita nazo manyazi? Zinthu zimenezo zotsatira zake ndi imfa! 22 Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha. 23 Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.